Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


38 Mau a Mulungu Okhudza Kumvera Olamulira

38 Mau a Mulungu Okhudza Kumvera Olamulira

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, tili ndi udindo wotsatira malamulo a Mulungu omwe ali m'Malemba Opatulika.

Kutsatira malamulo amenewa kumaphatikizapo kumvera olamulira athu, anthu omwe ali pafupi nafe kuti atiphunzitse ndikutitsogolera, kaya kutchalitchi, kunyumba, kuntchito kapena kudziko lathu lonse. Tikamachita izi, tikutsatira mfundo yofunika kwambiri imene Mulungu anatipatsa m’Mawu ake, chifukwa kumvera Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse.

Kumvera olamulira athu kudzatibweretsera madalitso ambiri m'miyoyo yathu, ndikutithandiza kukula mbali zonse, chifukwa khalidwe lathu lidzalimbitsidwa ndipo tidzakhala okonzeka kulandira zambiri kuposa zomwe talandirapo kale. Mulungu amadalitsa anthu omwe amatsatira chifuniro chake ndikulemekeza malamulo ake.

Choncho, n’kofunika kulemekeza olamulira athu mwa kuwapempherera kapena m’njira ina iliyonse yabwino yosonyeza ulemu.




Eksodo 22:28

Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:12

Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:21

Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe, osadudukira anthu osinthasintha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 8:2-5

Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu. Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda. Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani? Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:7

Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:21

Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:2-3

nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose; Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake. Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama, chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:1-3

Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa; koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso. chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse. Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo. Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:3-4

Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo: pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:13-14

Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:3-5

Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo: pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:40

Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:22

Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:5-8

Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu; si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai; podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:15

Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14-15

Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 2:21

pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:22-24

Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye; chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3-4

Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:2

Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:5

Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1

Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:1-2

Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino; Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize, podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha. Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu. Zena nkhoswe ya milandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu, Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso. Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m'chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse. asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:17

Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:1-2

Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa; koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso. chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:28

Pakuti ufumuwo ngwa Yehova; Iye achita ufumu mwa amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-4

Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo. Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga. Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo: pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:1

Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:13-15

Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:18

Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate, Inu ndinu Wamphamvuyonse, muli ndi ulamuliro pa zonse, chifukwa ndinu Woyera ndi Wokwezeka. Ndikupempha kuti atsogoleri ndi akuluakulu a maboma adziwe kuti Inu ndinu Mfumu ya mafumu, ndipo agonjetse ulamuliro wawo pansi pa chitsogozo cha Mzimu Woyera wanu, ndipo ndi nzeru zanu azilamulira mitundu yonse mwachilungamo. Mawu anu amati: "Aliyense agonjere olamulira akuluakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu, ndipo uliwonse umene ulipo, Mulungu ndiye anauuika." Ambuye, mundiphunzitse kugonjera olamulira amene mwaiika pa moyo wanga, onse a dziko lapansi ndi auzimu. Mtima wanga ukhale womvera, wokonzeka kulandira uphungu, osakana, koma uzindikire olamulira amene inu mwaiika, kaya panyumba, kuntchito, kutchalitchi, kapena kudziko. Mundiphunzitse kusonyeza nthawi zonse mzimu womvera ndi kukhala chitsanzo kwa iwo amene ali pafupi nane, chifukwadi mu kumvera muli madalitso anga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa