Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Tito 1:5 - Buku Lopatulika

5 Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira.

Onani mutuwo Koperani




Tito 1:5
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, naimirira mu utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.


Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.


Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m'tsogolo.


natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.


ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo.


Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.


ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu.


Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.


Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.


Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.


Ndipo m'mene tidapita pang'onopang'ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone;


Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.


Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.


Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.


Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.


Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,


Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.


Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zilombo zoipa, aumbombo, aulesi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa