Yoswa 16 - Buku LopatulikaMalire a Efuremu 1 Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele; 2 natuluka ku Betele kunka ku Luzi, napitirira kunka ku malire a Aariki, ku Ataroti; 3 natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja. 4 Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao, 5 Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda; 6 natuluka malire kumadzulo ku Mikametati kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kunka ku Taanatisilo, naupitirira kum'mawa kwake kwa Yanowa: 7 natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani. 8 Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao; 9 pamodzi ndi mizinda adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, mizinda yonse pamodzi ndi midzi yao. 10 Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi