Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 7:2 - Buku Lopatulika

Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu a ku Betele anali atatuma Sarezere ndi Regemumeleki ndi anthu ao, kuti akapemphe chifundo kwa Chauta.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova

Onani mutuwo



Zekariya 7:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.


Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.


kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.


Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?


Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.


Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.


Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,


ndi okhala m'mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.


chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.