Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 6:10 - Buku Lopatulika

10 Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Ulandire mphatso kwa anthu aŵa: Heledai, Tobiya, ndi Yedaya, amene abwerako ku ukapolo wa ku Babiloni. Iweyo upite tsiku lomwelo kwa Yosiya mwana wa Zefaniya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 6:10
7 Mawu Ofanana  

Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;


Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.


Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa