Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 8:21 - Buku Lopatulika

21 ndi okhala m'mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 ndi okhala m'mudzi umodzi adzamuka kumudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Anthu a mzinda wina adzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe chifundo kwa Chauta, tikapembedze Chauta Wamphamvuzonse. Ifeyo tikupita komweko.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:21
10 Mawu Ofanana  

Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.


Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.


Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.


Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.


Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.


Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova,


Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.


Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa