Yeremiya 26:19 - Buku Lopatulika19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Nanga kodi mfumu Hezekiya ndi anthu onse a ku Yuda adamupha amene uja? Kodi suja mfumu idaopa Chauta nipempha kuti aikomere mtima? Ndipo suja Chauta adaleka osaŵapatsa chilango chimene adaati aŵalange nacho? Koma ife tili pafupi kudziitanira tsoka lalikulu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!” Onani mutuwo |