Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
Yoweli 2:9 - Buku Lopatulika Alumphira mzinda, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akuulumphira mzindawo, akukwera pamwamba pa malinga. Akuloŵa m'nyumba, akuloŵera pa windo ngati mbala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala. |
Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.
Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.