Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:21 - Buku Lopatulika

21 Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Imfa yatifikira kudzera m'mawindo, yaloŵa ngakhale m'nyumba zathu zaufumu. Idapha ana athu m'miseu, ndipo idatha anyamata m'mabwalo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa; yapha ana athu mʼmisewu, ndi achinyamata athu mʼmabwalo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:21
17 Mawu Ofanana  

Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:


Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.


Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.


Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;


Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndi anthu ankhondo ake onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.


Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.


Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.


Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Alumphira mzinda, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu.


Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa.


Ndipo kudzachitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa.


Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa