Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m'dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba.
Yoweli 2:8 - Buku Lopatulika Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sakukankhanakankhana, aliyense akuyenda molunjika. Akupyola pakati pa zida zankhondo, osaŵaimitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo sakankhanakankhana, aliyense amayenda molunjika. Amadutsa malo otchingidwa popanda kumwazikana. |
Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m'dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba.
Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.
Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida;
Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.
palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka;
Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m'mabande ao.