Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 32:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Hezekiya adalimba mtima, nayamba kumanganso khoma limene linali litagamuka. Tsono adamanganso nsanja pakhomapo, ndiponso ina kunja kwake. Adalimbitsanso linga lotchedwa Milo ku mzinda wa Davide. Adapanga zida zankhondo ndi zishango zambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kenaka iye anagwira ntchito molimbika kukonza madera ogumuka a khoma ndi kumangapo msanja. Anamanganso mpanda wina kunja kwa mpanda winawo ndipo anamanga zolimbitsa Milo ku mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 32:5
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Ndipo chifukwa chakukweza iye dzanja lake pa mfumu ndi chimenechi: Solomoni anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mzinda wa Davide atate wake.


Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.


Ndipo anyamata ake ananyamuka, napangana, nakantha Yowasi kunyumba ya Milo potsikira ku Sila.


Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.


Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.


Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.


Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.


Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lake linabuka mpaka polowera ku Ejipito; pakuti analimbika chilimbikire.


Chitatha ichi tsono iye anaumangira mzinda wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa Chipata cha Nsomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'mizinda yonse yamalinga ya mu Yuda.


Wosalamulira mtima wake akunga mzinda wopasuka wopanda linga.


Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mzinda usiku, panjira pamunda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira panjira ya kuchidikha.


Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao.


Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili mu Sekemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa