Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 4:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Motero ine, anzanga, antchito anga, ndiponso anthu otitchinjiriza amene ankanditsata, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene ankavula zovala zake usiku pogona. Aliyense ankasunga chida chankhondo pambalipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Choncho ine, anzanga, antchito anga, ndi anthu otiteteza amene ankanditsata panalibe ndi mmodzi yemwe anavula zovala zake pogona. Aliyense anasunga chida chake chankhondo pambali pake.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 4:23
8 Mawu Ofanana  

Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone mu Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana.


Pamenepo panamveka kulira kwakukulu kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.


Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.


ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.


Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'madera ake, mu Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.


Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa