Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
Yoweli 1:3 - Buku Lopatulika Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muŵauze ana anu, iwowo auze ana ao, ndipo anawo aziwuzanso ana ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muwafotokozere ana anu, ndipo ana anuwo afotokozere ana awo, ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo. |
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;
Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.
ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.