Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:2 - Buku Lopatulika

2 Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Inu akuluakulu, mverani. Tcherani khutu, inu nonse okhala m'dziko. Kodi zoterezi zidaonekapo nthaŵi yanu kapena nthaŵi ya makolo anu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inu akuluakulu, imvani izi; mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko. Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu, kapena mʼnthawi ya makolo anu?

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:2
24 Mawu Ofanana  

Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha.


Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa, akuposa atate wako masiku ao.


Oipa akhaliranji ndi moyo, nakalamba, nalemera kwakukulu?


Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo, nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.


Dzamveni kuno, anthu inu nonse; tcherani khutu, inu nonse amakono,


Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.


Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;


Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.


Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti,


Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.


Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?


Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.


Amene ali ndi makutu, amve.


pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa