Yohane 3:7 - Buku Lopatulika Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usadabwe m'mene ndakuuza kuti muyenera kubadwanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ |
Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.
Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu.
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika;
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.