Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.
Yohane 20:2 - Buku Lopatulika Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!” |
Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.
Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!
Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye.
Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa.
Petro, m'mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?
Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni za izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja.