Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 20:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti kufikira pomwepo sanadziwe lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 (Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).

Onani mutuwo Koperani




Yohane 20:9
22 Mawu Ofanana  

Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa padziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.


Kodi sanayenere Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?


Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.


Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.


natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa