Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 21:7 - Buku Lopatulika

7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 21:7
20 Mawu Ofanana  

Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu.


Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu.


Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.


Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.


Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.


Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!


Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye.


Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye.


Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.


Petro, m'mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?


Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni za izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.


Koma ophunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.


Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.


Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;


Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa