Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 21:6 - Buku Lopatulika

6 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Yesu adaŵauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 21:6
8 Mawu Ofanana  

mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja.


Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.


ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.


Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa