Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
Yohane 19:2 - Buku Lopatulika Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono asilikali adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake. Adamuveka chovala chofiirira, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Asilikali analuka nkhata yaminga ndi kumuveka pamutu pake. Kenaka anamuveka mkanjo wapepo |
Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.
Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!