Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni.
Yohane 13:7 - Buku Lopatulika Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuyankha kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziŵa tsopano, koma udzazidziŵa m'tsogolo muno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.” |
Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni.
Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.
Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?
Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.
Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe.
Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.