Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:16 - Buku Lopatulika

16 Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Izi sanazidziwa ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pa nthaŵi imeneyo ophunzira ake sadazimvetse zimenezo. Koma Yesu atauka ndi ulemerero, iwo adakumbukira kuti zimenezi zidalembedwa kunena za Iye, ndipo kuti adamchitiradi zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:16
19 Mawu Ofanana  

Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.


Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;


Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.


Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.


Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.


Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.


Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.


Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.


Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu mu Kumwamba,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa