Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m'ndende yenseyo, wachotsedwa m'nsinga.
Obadiya 1:20 - Buku Lopatulika Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala mu Sefaradi adzakhala nayo mizinda ya kumwera, cholowa chao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwera, cholowa chao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli amene ali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati; a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda ya ku Negevi. |
Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m'ndende yenseyo, wachotsedwa m'nsinga.
Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.
M'mizinda ya kumtunda, m'mizinda ya kuchidikha, m'mizinda ya kumwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'mizinda ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.
pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.
Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao.
ndipo Eliya sanatumidwe kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye.