Yeremiya 32:44 - Buku Lopatulika44 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201444 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kuchidikha, ndi m'midzi ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa44 Anthu adzaguladi minda ndi ndalama. Mapangano ake adzalembedwa, adzamatidwa ndipo padzakhala umboni wake ku dera la Benjamini, ku malo oyandikana ndi Yerusalemu, m'mizinda ya ku Yuda, m'mizinda yakumapiri, m'mizinda yakuchigwa ndi yakumwera ku Negebu. Zoona, ndidzaŵabwezera ufulu wao,” akuterotu Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero44 Adzagula minda ndi ndalama zasiliva, ndipo achita pangano, ndi kumata pamaso pa mboni. Izi zidzachitika mʼdziko la Benjamini, ku malo ozungulira Yerusalemu, mʼmizinda ya Yuda, mʼmizinda ya ku mapiri, mʼmizinda ya kuchigwa ndi yakummwera ku Negevi. Zoona, ndidzabwezera ufulu wawo, akutero Yehova.” Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.