Yeremiya 13:19 - Buku Lopatulika19 Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m'ndende yenseyo, wachotsedwa m'nsinga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Midzi ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wachotsedwa m'ndende wonsewo, wachotsedwa m'nsinga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Mizinda yanu ya ku Negebu aitsekera kunja, palibe wina woti nkuitsekula. Yuda yense watengedwa ukapolo, watengedwa yense ukapolo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo, watengedwa yense ukapolo. Onani mutuwo |
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.