Numeri 9:19 - Buku Lopatulika Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa Kachisi, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihemacho, Aisraele ankasungabe lamulo la Chauta, ndipo sankanyamuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtambowo ukakhala pa chihema nthawi yayitali, Aisraeli ankasungabe lamulo la Yehova ndipo iwo sankasamukanso. |
Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi.
Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa chihema amakhala m'chigono.
Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.