Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Numeri 9:12 - Buku Lopatulika Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asasiyeko nyamayo mpaka m'maŵa kapena kuphwanya mafupa ake. Achite Paskayo potsata malamulo ake onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse. |
Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.
Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;
Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.
Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.
Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.