Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:3 - Buku Lopatulika

3 Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:3
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.


Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.


Pamenepo Yosiya anachitira Yehova Paska mu Yerusalemu, naphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti,


Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, pali Paska wa Yehova.


Ana a Israele achite Paska pa nyengo yoikidwa.


Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, kuti achite Paska.


chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa