Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:36 - Buku Lopatulika

36 Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Zinthu izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe: “Palibe limodzi la mafupa limene lidzathyoledwa,”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:36
10 Mawu Ofanana  

Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.


Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoke limodzi lonse.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Audye m'nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.


Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska.


Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,


Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.


Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi.


Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa