choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;
Numeri 8:3 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose. |
choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;
Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.
Ndipo mapangidwe ake a choikaponyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikaponyali.
Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.