Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:3
5 Mawu Ofanana  

choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo;


Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.


“Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.”


Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose.


Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa