Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:15 - Buku Lopatulika

15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:15
10 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;


Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.


Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake?


Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.


Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.


Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.


kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,


Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa