Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:2 - Buku Lopatulika

2 Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikapo nyalicho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza Aroni kuti, pamene ukuika nyale, uike zisanu ndi ziŵiri, ndipo ziwunikire patsogolo pa choikaponyale.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:2
19 Mawu Ofanana  

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.


Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.


Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.


Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.


choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;


Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Akonze nyalizo pa choikaponyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose.


Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.


Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.


Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;


Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa