ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Numeri 8:11 - Buku Lopatulika ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Aroni apereke Aleviwo pamaso pa Chauta, kuti akhale chopereka choweyula cha Aisraele, kuti ntchito ya Alevi ikhaledi yotumikira Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova. |
ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.
anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.
ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.
Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.