Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:24 - Buku Lopatulika

24 ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Chakudya chonsechi uchiike m'manja mwa Aroni ndi mwa ana ake, ndipo iwowo achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:24
9 Mawu Ofanana  

ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosakaniza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;


Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.


ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.


adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.


Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa