Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:25 - Buku Lopatulika

25 Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Kenaka uchotse zonsezo m'manja mwao, ndipo uzipsereze pa guwa, pamwamba penipeni pa zopereka zija kuti zipereke fungo lokondweretsa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:25
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.


Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero.


Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.


Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yopalamula.


Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Kodi sindinasankhule iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe paguwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatse banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa