Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Utenge nganga ya nkhosa yamphongo imene adaipha podzoza Aroni, ndipo uiweyule kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Imeneyi ndiyo idzakhala gawo lako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:26
8 Mawu Ofanana  

Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.


Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;


ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo paguwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.


Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.


Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa