Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:30 - Buku Lopatulika

30 adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 atengeko ndi manja ake zigawo zoyenera kuzitentha, zopereka kwa Chauta, ndiye kuti mafuta ndi nganga yomwe. Tsono ngangayo aiweyule kuti ikhale chopereka choweyula kwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:30
16 Mawu Ofanana  

Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.


Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nao pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako aamuna, mwa lemba losatha; monga Yehova analamula.


Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.


ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo paguwa la nsembe.


Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose.


ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.


ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.


Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa