Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pambuyo pake Alevi asanjike manja ao pamitu ya ng'ombe zamphongo, ndipo iwe upereke kwa Chauta ng'ombe imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Inayo uipereke kuti ikhale nsembe yopsereza, kuchitira mwambo wopepesera machimo a Alevi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:12
25 Mawu Ofanana  

Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.


Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.


ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;


ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.


Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.


nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.


Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.


Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.


Monga anachita lero lino, momwemo Yehova analamula kuchita, kukuchitirani chotetezera.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova analamula.


pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;


Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yake yauchimo, ndi nsembe yake yopsereza;


Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova.


Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosakaniza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo.


Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa