zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.
Numeri 7:79 - Buku Lopatulika chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; |
zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.
Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;
Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake aang'ono, amweremo.
Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.