Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 1:9 - Buku Lopatulika

9 Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chiŵerengero chake chinali chotere: Mabeseni agolide 30 a zopereka, mabeseni asiliva 1,000 a zopereka, zofukizira 29,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chiwerengerochi chinali motere: Mabeseni agolide 30 mabeseni asiliva 1,000 a zopereka 29

Onani mutuwo Koperani




Ezara 1:9
14 Mawu Ofanana  

ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.


Ndi zopalira moto, ndi mbale zowazira za golide yekhayekha, ndi zasiliva yekhayekha, mkulu wa asilikali anazichotsa.


Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.


Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu:


Anapanganso magome khumi, nawaika mu Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.


zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.


Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi,


ndi zikho zagolide makumi awiri za madariki chikwi chimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golide.


Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwake kwa siliva ndi golide ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.


chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;


Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa