Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 7:3 - Buku Lopatulika

anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga awiru anapereka galeta ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa chihema.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema.

Onani mutuwo



Numeri 7:3
7 Mawu Ofanana  

Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.


Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.


Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.


Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova.


Taonani, ndidzakupsinjani m'malo mwanu, monga lipsinja galeta lodzala ndi mitolo fwaa.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,