Numeri 7:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga awiru anapereka galeta ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa chihema. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta. Onani mutuwo |
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.