Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsiku lomwelo akulu a Aisraele, ndiye kuti atsogoleri a mabanja ndi a mafuko amene ankayang'anira kuŵerenga kuja,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:2
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide.


Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300.


Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa.


Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi:


Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa