Numeri 7:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa Kachisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pa tsiku limene Mose adamaliza kumangitsa chihema cha Mulungu, nachidzoza ndi kuchipatula, pamodzi ndi zipangizo zake, adadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziŵiya zake zomwe. Onani mutuwo |
Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.