Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.
Numeri 4:8 - Buku Lopatulika Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pamwamba pa zimenezo ayalepo nsalu yofiira, ndi kuziphimba zonsezo ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mphiko m'zigwinjiri zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake. |
Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikaponyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake.