Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:
Numeri 34:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose kuti, |
Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:
Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.
Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.
Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.
Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;
Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake,