Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:13 - Buku Lopatulika

13 Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana amuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Tsono iwowo adati, “Mbuyathu, ife tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri pachibale pathu, bambo wathu mmodzi, ku dziko la kwathu ku Kanani. Wamng'ono ali ndi bambo wathu, ndipo wina adamwalira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma iwo anayankha, “Tinalipo ana aamuna khumi ndi awiri. Abambo athu ndi mmodzi, ndipo kwathu ndi ku Kanaani. Panopo wotsiriza ali ndi abambo athu ndipo wina anamwalira.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:13
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?


Tonse tili ana aamuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda.


Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.


tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.


Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.


Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?


Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.


wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;


Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


Atate athu anachimwa, kulibe iwo; ndipo tanyamula mphulupulu zao.


Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa