Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.
Numeri 32:4 - Buku Lopatulika dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa dziko limene Chauta adagonjetsera Aisraele, ndi dziko loyenera kuŵeterako ng'ombe, ndipo atumiki anufe tili ndi ng'ombe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto. |
Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.
Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi mu Giliyadi.
Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.
Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.
Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.
Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.
kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.