1 Mbiri 4:41 - Buku Lopatulika41 Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Anthu a fuko a Simeoniwo, ochita kulembedwa maina, adadza pa nthaŵi ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, ndipo adaononga mahema a Ahamuwo ndi kupha Ameuni amene adaŵapeza kumeneko. Adaonongeratu anthu onsewo kotero kuti dzina lao silidamvekenso mpaka lero lino. Kenaka iwowo adakhala ku malo amenewo, popeza kuti kunali msipu womadyetsako ziweto zao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. Onani mutuwo |